Isaiah 44:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndani nanga akulingana ndi Ine? Aimirire, alankhule, andifotokozere. Kuyambira kalekale ndani adalosa zakutsogolo? Atidziŵitsetu zimene zikudzachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m'tsogolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule. Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale, ndi ziti zimene zidzachitike; inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ici ndi kundilongosolera ici, cikhazikitsire Ine anthu akale? milunguyo iwadziwitse zomwe zirinkudza, ndi za m'tsogolo.