Isaiah 45:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akulankhula ndi wodzozedwa wake Kirusi amene adamgwira dzanja lamanja, kuti agonjetse mitundu ina ya anthu, aŵathe mphamvu mafumu, ndi kutsekula zitseko kuti zipata zisatsekeke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake Koresi amene anamugwira dzanja lamanja kuti agonjetse mitundu ya anthu ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo, ndi kutsekula zitseko kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova kwa wodzozedwa wace kwa Koresi, amene dzanja lace lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pace, ndipo ndidzamasula m'cuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pace, ndi zipata sizidzatsekedwa: