Isaiah 45:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine amene ndidautsa Kirusi kuti chilungamo chichitike. Ndidzaongola mseu uliwonse umene adzadzeramo. Adzamanganso mzinda wanga wa Yerusalemu ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, osapereka ndalama kapena mphotho,” watero Chauta Mphambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndautsa Kirusi m'chilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zake zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwaufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe: ndipo ndidzawongolera njira zake zonse. Iye adzamanganso mzinda wanga ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, wopanda kupereka ndalama kapena mphotho, akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndautsa Koresi m'cilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zace zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwa ufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.