Isaiah 45:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuuza Aisraele kuti, “Chuma cha ku Ejipito ndi malonda a ku Etiopiya zidzakhala zanu. Anthu a ku Saba, a msinkhu aatali, adzabwera kwa inu ndi kukhala akapolo anu ndipo azidzakutsatani. Adzabwera ali omangidwa ndi maunyolo, ndi kukugwadirani. Adzakupembani ndi kunena kuti, ‘Mulungu ali ndi inu nokha, palibenso wina ai. Kupatula Iyeyo palibe mulungu wina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu. Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba adzabwera kwa inu ndipo adzakhala anthu anu; iwo adzidzakutsatani pambuyo panu ali mʼmaunyolo. Adzakugwadirani ndi kukupemphani, ponena kuti, ‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina; palibenso mulungu wina.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Nchito ya Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.