Isaiah 45:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Israele amampulumutsa ndi Chauta, ndipo chipulumutso chake chidzakhalapo mpaka muyaya, Anthu ake sadzaŵachititsa manyazi konse, sadzakhala onyozeka konse.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova adzapulumutsa Israeli ndi chipulumutso chamuyaya; simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Israyeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi cipulumutso cosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru ku nthawi zosatha.