Isaiah 45:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwacabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.