Isaiah 45:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidalankhule mwachinsinsi pa malo ena m'dziko lamdima. Sindidauze zidzukulu za Yakobe kuti zizindifunafuna kumene kuli kopanda kanthu. Ine Chauta ndimalankhula zoona, ndimanena zolungama.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindinayankhule mwachinsinsi, pamalo ena a mdima; Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti, “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.” Ine Yehova, ndimayankhula zoona; ndikunena zolungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwacabe; Ine Yehova ndinena cilungamo, ndinena zimene ziri zoona.