Isaiah 45:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kambani, fotokozani mlandu wanu. Mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani adaneneratu zimene zidzachitika? Ndani adaloseratu kalekale zimenezo? Kodi si Ineyo, Chautane? Ndithu, kupatula Ine palibe Mulungu wina, Mulungu wachilungamo ndi wopulumutsa. Palibenso wina aliyense kupatula Ine.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Fotokozani mlandu wanu, mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale? Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana? Kodi si Ineyo Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine, Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa, palibenso wina kupatula Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenani inu, turutsani mlandu wanu; inde, acite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ici ciyambire nthawi yakale? ndani wanena ici kale? kodi si ndine Yehova? ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.