Isaiah 45:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndalumbira dzina langa lomwe, pakamwa panga palankhula moona mau amene sadzasinthika konse, akuti, ‘Bondo lililonse lidzandigwadira, anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndalumbira ndekha, pakamwa panga patulutsa mawu owona, mawu amene sadzasinthika konse akuti, bondo lililonse lidzagwada pamaso panga; anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndadzilumbira ndekha, mau acokera m'kamwa mwanga m'cilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.