Isaiah 45:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima, katundu wa pamalo obisika, kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzakupatsa iwe cuma ca mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israyeli.