Isaiah 45:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobe, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israele, ndikukuitana potchula dzina lako, ndikukupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli, Ine ndakuyitana pokutchula dzina ndipo ndakupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakuitana iwe dzina lako, cifukwa ca Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.