Isaiah 45:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina; kupatula Ine palibenso Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu, ngakhale sukundidziwa Ine,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;