Isaiah 45:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha. Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti anthu akadziwe kucokera ku maturukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.