Isaiah 45:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa amene amakangana ndi mlengi wake, ngakhale ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi mtapo ungafunse munthu woumba kuti, “Kodi ukuumba chiyani?” Kapena kunena kuti, “Woumbawe, ulibe luso!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! Phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani? Pena ntchito yako, Iye alibe manja?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake, ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti, ‘Kodi ukuwumba chiyani?’ Kodi ntchito yako inganene kuti, ‘Ulibe luso?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wace! phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga ciani? pena nchito yako, Iye alibe manja?