Isaiah 46:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayu Beli wapendekeka, Nebo waŵerama! Mafano ameneŵa a Babiloni aŵaika pa abulu ndi ng'ombe. Zinthu zimene kale munkanyamula ndinu, tsopano mukuziika ngati katundu wolemera pamsana pa nyama zotopa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Beli wagwada pansi, Nebo wawerama; nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo. Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe. Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.