Isaiah 46:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse;