Isaiah 46:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuitana chiwombankhanga kuchokera kuvuma, ndiye kuti munthu wofumira ku dziko lakutali, amene adzapherezetsa zimene ndikufuna kuchita. Zimene ndalankhula, ndidzazifitsa, zimene ndafuna kuchita ndidzazichitadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa. Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa. Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi; zimene ndafuna ndidzazichitadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.