Isaiah 46:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena amatsekula zikwama zao namatulutsamo golide, ndipo amayesa siliva pa masikelo. Amalemba mmisiri wosula, ndipo iye amaŵapangira milungu. Kenaka iwowo amagwada pansi, namaipembedza milunguyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene ataya golidi, namturutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golidi; iye napanga nazo mlungu; iwo agwada pansi, inde alambira.