Isaiah 46:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amainyamula pa mapewa ao, naisenza. Amaikhazika pamalo pake nikhala pomwepo, ndipo singathe kusuntha pamalo pakepo. Wina aliyense akapemphera kwa milunguyo, siyankha, kapena kumpulumutsa ku mavuto ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwace, nukhala ciriri; pamalo pacepo sudzasunthika; inde, wina adzaupfuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zobvuta zace.