Isaiah 47:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Iwe namwali, Babiloni, tsika ndi kukhala pa fumbi. Iwe namwali, Kaldeya, khala pansi, opanda mpando waufumu. Pakuti sadzakutchulanso wofeŵa ndi wodzitekemeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsika, ndi kukhala pa fumbi, iwe namwali, Babuloni; khala pansi wopanda mpando waufumu, iwe namwali, Kaldeya pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera kumugwira mosamala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsika, ukhale m'pfumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babulo; khala pansi popanda mpando wacifumu, mwana wamkazi wa Akasidi, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.