Isaiah 47:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Sunkada nako nkhaŵa konse kuipa kwako, unkaganiza kuti palibe wokupenya. Kuchenjera kwako ndi nzeru zako zidakusokeza, ndipo mumtima mwako unkaganiza kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe unkadalira kuyipa kwako ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi cidziwitso cako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina.