Isaiah 47:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira nchito ciyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.