Isaiah 47:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera.