Isaiah 47:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵakwiyira anthu anga, ndidaŵanyoza ngati si anthu anga. Ndidaŵapereka m'manja mwako, ndipo iwe sudaŵachitire chifundo. Udaumira mtima ndi nkhalamba zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawakwiyira anthu anga, osawasamalanso. Ndinawapereka manja mwako, ndipo iwe sunawachitire chifundo. Iwe unachitira nkhanza ngakhale nkhalamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa colowa canga, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera cifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.