Isaiah 47:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unkaganiza kuti nthaŵi zonse udzakhala mfumukazi, mwakuti zinthu zimenezi sudazisamale, sudaganizirenso m'mene zidzathere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse ngati mfumukazi.’ Koma sunaganizire zinthu izi kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira comarizira cace.