Isaiah 47:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake tsono umvetsere izi, iwe wongokonda zokondweretsawe, iwe amene umakhala pabwino, numaganiza mumtima mwako kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai. Sindidzakhala konse wamasiye, ndipo ana anga sadzafa.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, amene ukukhala mosatekesekawe, umaganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, ndipo ana anga sadzamwalira.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, imva ici, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;