Isaiah 47:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma m'kamphindi, tsiku limodzi, zinthu ziŵiri zonsezi zidzakugwera. Ana ako onse kukufera, iweyo kusanduka wamasiye, zonsezo zidzakugwera pamodzi, ngakhale kuti uli ndi matsenga ambiri ndi zithumwa zamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu ngakhale ali ndi amatsenga ambiri ndi mawula amphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa unyinji wa matsenga ako, ndi pakati pa maphenda ako ambirimbiri.