Isaiah 48:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mverani izi inu a banja la Yakobe, inu amene dzina lanu amakutchulani Aisraele, inu zidzukulu za Yuda. Inu mumalumbira dzina la Chauta, ndipo mumapemphera kwa Mulungu wa Israele, pamene zimenezo sizichokera mu mtima woona ndi wolungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo, inu amene amakutchani dzina lanu Israeli, ndinu a fuko la Yuda, inu mumalumbira mʼdzina la Yehova, ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli, ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani inu ici, banja la Yakobo, amene muchedwa ndi dzina la Israyeli, amene munaturuka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kuchula dzina la Mulungu wa Israyeli, koma si m'zoona, pena m'cilungamo.