Isaiah 48:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Sonkhanani nonsenu, ndipo mumvetsere. Mwa milungu ina ndani adalosapo zimenezi? Amene Chauta amamkonda uja adzachita zomwe Chautayo adakonzera Babiloni, ndi dzanja lake lamphamvu adzalimbana ndi Akaldeya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani: Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi? Wokondedwa wa Yehova uja adzachita zomwe Iye anakonzera Babuloni; dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzacita kufuna kwace pa Babulo, ndi mkono wace udzakhala pa Akasidi.