Isaiah 48:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsa kuti upindule, ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israyeli, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.