Isaiah 48:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuuza Israele kuti, “Zimene zidachitika poyamba ndidaaloseratu kalekale, zidaatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndidaazilengeza. Tsono mwadzidzidzi ndidachitapo kanthu, ndipo zidaonekadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale, zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza; tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinaturuka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazicita izo, ndipo zinaoneka.