Isaiah 48:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaakuuziratu zakutsogolo kalekale. Zisanachitike ndidaazilengezeratu kwa iwe, kuti usadzanene kuti, ‘Fano langa ndilo lidachita zimenezi, fano langa losema ndi fano langa loumba ndiwo adalamula kuti zichitike!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe; zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe kuti unganene kuti, ‘Fano langa ndilo lachita zimenezi, kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace ndinakudziwitsa ici kuyambira kale; cisanaoneke ndinakusonyeza ico, kuti iwe unganene, Fano langa lacita izo, ndi cifanizito canga cosema, ndi cifaniziro canga coyenga zinazilamulira.