Isaiah 48:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikhalire sudamve chikhalire sudadziŵe, nkale lonse makutu ako sanali otsekuka. Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu, ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako adakutchula waupandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa; makutu anu sanali otsekuka. Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde, kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wacita mwaciwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa cibadwire.