Isaiah 49:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kuzambwe, enanso adzachokera ku Asuwani kumwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kumadzulo, enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, awa adzacokera kutari; ndipo taonani, awa ocokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ocokera ku dziko la Sinimu.