Isaiah 49:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uyang'ane pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Anthu ako onse akusonkhana, akubwera kwa iwe. Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo, anthu ako adzakhala chinthu chokukongoletsa. Udzaŵaonetsera monga amachitira mkwati wamkazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tukula maso ako kuunguzaunguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadziveka wekha ndi iwo onse, monga ndi chokometsera, ndi kudzimangira nao m'chuuno ngati mkwatibwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe. Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo, anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tukula maso ako kuunguza-unguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadzibveka wekha ndi iwo onse, monga ndi cokometsera, ndi kudzimangira nao m'cuuno ngati mkwatibwi.