Isaiah 49:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithudi, iwe amene wasanduka bwinja, amene udaasiyidwa ndi kusakazika, tsopano udzaŵachepera anthu odzakhala mwa iwe. Ndipo amene adakuwononga aja adzaŵapirikitsira kutali ndi iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, kunena za malo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wochepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa ndipo dziko lako ndi kusakazidwa, chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, kunena za tnalo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wocepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutari.