Isaiah 49:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani adandiberekera ana aŵa? Ana anga onse adamwalira ndipo sindidanthenso kukhala ndi ana ena. Ndidaali ku ukapolo, ndidaaiŵalika. Nanga ndani adaŵalera ana ameneŵa? Ndidaatsala ndekha. Nanga ana ameneŵa adachokera kuti?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa? Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena; ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa. Ndani anawalera ana amenewa? Ndinatsala ndekha, nanga awa, achokera kuti?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anacotsedwa kwa ine, ndipo ndiri wouma, ndi wocotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?