Isaiah 49:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye Chauta akunena kuti, “Ndidzakodola anthu a mitundu ina. Ndidzaŵakwezera mbendera kuti adzabwere. Tsono adzabwera nawo ana ako aamuna ataŵatengera m'manja, ndiponso ana ako aakazi, ataŵasenzera pa mapewa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako amuna pa chifuwa chao, ndi ana ako akazi adzatengedwa pa mapewa ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi, “Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere. Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere. Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako amuna pa cifuwa cao, ndi ana ako akazi adzatengedwa pa mapewa ao.