Isaiah 49:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu adzakhala ngati atate okulerani, akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani. Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani. Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao akulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu adzakhala abambo wongokulera ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera. Iwo adzagwetsa nkhope zawo pansi. Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova; iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao akuru adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka pfumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.