Isaiah 49:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe; adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu, Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yao yao; ndi mwazi wao wao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndiri Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.