Isaiah 49:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu. Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.” Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta, mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinati, Ndagwira ntchito mwachabe, ndatha mphamvu zanga pachabe, ndi mopanda pake; koma ndithu chiweruziro changa chili ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe, koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova, ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.