Isaiah 49:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndi amene adandiwumba m'mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye, ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye. Choncho ndimalemekezeka m'maso mwa Chauta, ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wake, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israele asonkhanidwe kwa Iye; chifukwa Ine ndili wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwumba ine mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye, choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova, ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;