Isaiah 49:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mpulumutsi ndi Woyera uja wa Israele, akulankhula ndi wonyozedwa kwambiri uja, wodedwa ndi mitundu ina ya anthu, kapolo wa mafumu ankhanza. Akunena kuti, “Mafumu adzaimirira mwaulemu poona iwe, akalonga nawonso adzadziponya pansi chafufumimba. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Chauta, amene ali wokhulupirika, Woyera uja wa Israele, amene adakusankhula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula, Woyerayo wa Israeli akunena, amene mitundu ya anthu inamuda, amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti, “Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira. Akalonga nawonso adzagwada pansi. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Mombolo wa Israyeli, ndi Woyera wace, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyansidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira cifukwa ca Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israyeli, amene anakusankha Iwe.