Isaiah 49:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza; ndinakusunga ndi kukusandutsa kuti ukhale pangano kwa anthu, kuti dziko libwerere mwakale ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la cipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;