Isaiah 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amangoimba zeze, pangwe, ng'oma ndi chitoliro, nkumamwa vinyo pa maphwando ao. Koma sasamala ntchito za Chauta, sapenya ntchito za manja ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe, matambolini, zitoliro ndi vinyo, ndipo sasamala ntchito za Yehova, salemekeza ntchito za manja ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zeze ndi mgoli, ndi lingaka ndi citoliro, ndi vinyo, ziri m'mapwando ao; koma iwo sapenyetsa nchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa macitidwe a manja ace.