Isaiah 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake kumanda sikukhuta, kwangoti kukamwa yasa kuti kulandire aliyense. Anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka, adzagweramo ali wowowo, m'kuledzera kwaoko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake; mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka; adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo manda akuza cilakolako cace, natsegula kukamwa kwace kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.