Isaiah 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama. Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.