Isaiah 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adautipula nachotsa miyala yonse, ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi. Adamanga nsanja pakati pa mundawo, nasema mopondera mphesa m'kati momwemo. Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ai, udabala mphesa zachabechabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iye anakumba mcerenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pace nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.