Isaiah 5:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto, momwemonso mizu yawo idzawola ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi; chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse, ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace monga ngati lilime la moto likutha ciputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wobvunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati pfumbi; cifukwa kuti iwo akana cilamulo ca Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israyeli.