Isaiah 5:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ukali wa Chauta waŵayakira anthu ake. Iye watambalitsa dzanja lake pa anthuwo kuti aŵakanthe. Mapiri agwedezeka, ndipo mitembo ya anthuwo yangoti mbwee ngati zinyalala pakati pa miseu. Koma ngakhale Mulungu watero, mkwiyo wake sudaleke, dzanja lake lidakali chitambalitsire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake; watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha Mapiri akugwedezeka, ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ace, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lace, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.